Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
Filemoni 1:9 - Buku Lopatulika koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m'ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu, |
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.
Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,
okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro.
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.