Filemoni 1:20 - Buku Lopatulika Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono, mbale wanga, inenso undithandizeko chifukwa cha Ambuye. Undisangulutseko ngati mbale mwa Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu. |
Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni?
Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.
Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?