Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Filemoni 1:19 - Buku Lopatulika

19 ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pano mau aŵa ndikulemba ndi dzanja langalanga kuti, “Ine Paulo ndidzalipira.” Nkosasoŵekera kukukumbutsa kuti paja iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wako womwe wachikhristuwu!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:19
14 Mawu Ofanana  

Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse:


Ine Tersio, ndilikulemba kalata ameneyu, ndikupereka moni mwa Ambuye.


Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;


kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.


Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.


Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.


kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.


Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wokongola kanthu, kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa