Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Filemoni 1:16 - Buku Lopatulika osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati mbale wokondedwa. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu mnzako ndiponso mkhristu mnzako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye. |
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu.
Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;
Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;
Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.