Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Filemoni 1:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati mbale wokondedwa. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu mnzako ndiponso mkhristu mnzako.

Onani mutuwo Koperani




Filemoni 1:16
10 Mawu Ofanana  

“Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale.


Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.”


Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu.


Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye.


Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu.


Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.


Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa