1 Timoteyo 6:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Amene ambuye ao ndi akhristu, asaŵapeputse poona kuti ndi abale. Kwenikweni aziŵatumikira koposa, popeza kuti amene amapindula ndi ntchito yao, nawonso ndi akhristu, ndiponso okondedwa. Uziŵaphunzitsa anthu ndi kuŵalamula ntchito zimenezi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu. Onani mutuwo |