Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Yohane 5:1 - Buku Lopatulika

1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 5:1
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.


Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa.


Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.


Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadze kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.


Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?


Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Iye amene akonda mbale wake akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.


Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.


Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.


Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?


Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sangathe kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.


M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;


Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.


Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.


Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa