Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.
Filemoni 1:13 - Buku Lopatulika Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikadakonda kuti akhalebe ndi ine kuno, kuti azinditumikira m'malo mwako, pokhala ndili m'ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino. |
Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu,