Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?
Eksodo 9:7 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite. |
Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?
Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai.
Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.
Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.
Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;
Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;