Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 9:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:7
11 Mawu Ofanana  

Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka. Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka?


Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza.


Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite.


Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.


Kenaka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Tapani phulusa la pa moto lodzaza dzanja ndipo Mose aliwaze mmwamba pamaso pa Farao.


Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.


Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve wa nkhongo gwaa, wa mutu wowuma.


Koma pamene inayamba kudzitama ndi kuwumitsa mtima wake ndi kuyamba kunyada, inachotsedwa pa mpando wake waufumu ndi kulandidwa ulemerero wake.


Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa