Eksodo 9:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. Onani mutuwo |