Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 9:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta waika nthaŵi, ndipo akunena kuti zimenezi azichita maŵa.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:5
10 Mawu Ofanana  

Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?


pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;


Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.


Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.


Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.


Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.


nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa