Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 9:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidzasiyanitsa pakati pa zoŵeta za Aisraele ndi za Aejipito. Motero palibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidzafe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:4
10 Mawu Ofanana  

sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao.


Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.


M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala.


Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu.


Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.


Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa