Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 9:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 9:6
10 Mawu Ofanana  

Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala, zoweta zawo ku zingʼaningʼani.


Analolera kukwiya, sanawapulumutse ku imfa koma anawapereka ku mliri.


“Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.


Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo.


“Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino.


Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse.


Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli.


Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.”


Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa