Eksodo 5:23 - Buku Lopatulika Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditse anthu anu konse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chipitire changa chija kwa Farao kukamuuza mau anu aja, wakhala akuzunzabe anthu anu. Ndipo Inu simudachitepo kanthu konse kuti muŵaombole anthu anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.” |
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;
Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.