Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 11:21 - Buku Lopatulika

21 Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Nchifukwa chake Chauta akunena za anthu a ku Anatoti amene afuna kuwononga moyo wanga namanena kuti, “Usalosenso m'dzina la Chauta kuti tingakuphe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:21
22 Mawu Ofanana  

amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;


Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.


ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za padziko lapansi.


Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.


Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake.


Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.


Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.


ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa