Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 5:23 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

23 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditse anthu anu konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Chipitire changa chija kwa Farao kukamuuza mau anu aja, wakhala akuzunzabe anthu anu. Ndipo Inu simudachitepo kanthu konse kuti muŵaombole anthu anu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:23
9 Mawu Ofanana  

Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’


Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova. Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.


Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.


Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”


Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri ngati maziko mu Ziyoni, mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.


“Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’


Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa