Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 5:22 - Buku Lopatulika

22 Pamenepo Mose anabwerera nanka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Choncho Mose adapemphera kwa Chauta nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Nanga ine mudanditumiranji?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mose anabwerera kwa Yehova ndipo anati, “Chonde Ambuye, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Kodi munanditumira zimenezi?

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.


Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.


Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?


Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani!


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa