Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
Eksodo 4:28 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Mose adafotokozera Aroni zonse zimene Chauta adaamuuza, pa nthaŵi imene ankamutuma. Adamuuzanso za zozizwitsa zonse zija zimene Chauta adamlamula kuti akachite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose anamufotokozera Aaroni chilichonse chimene Yehova anamutuma kuti akanene. Anamufotokozera za zizindikiro zozizwitsa zimene anamulamulira kuti akazichite. |
Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.
Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi: