Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yona 3:2 - Buku Lopatulika

2 Nyamuka, pita ku Ninive mzinda waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nyamuka, pita ku Ninive mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”

Onani mutuwo Koperani




Yona 3:2
13 Mawu Ofanana  

kukhazikitsa masiku awa a Purimu m'nyengo zao, m'mene Mordekai Myuda ndi mkazi wamkulu Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kufuula kwao.


Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira.


Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka.


Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo mvera mau otuluka m'kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti,


Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Ninive, monga mwa mau a Yehova. Koma Ninive ndiwo mzinda waukulu pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.


Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:


Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa