Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 4:2 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta adafunsa Moseyo kuti, “Kodi nchiyani chili m'manja mwakocho?” Mose adayankha kuti, “Ndodo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”

Onani mutuwo



Eksodo 4:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wauwisi wa libne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.


Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.


Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu.


Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo.


Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.


Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.


Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.