Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 30:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wauwisi wa libne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Tsono Yakobe adatenga nthambi zaziŵisi za mitengo ya mitundu itatu yakudzikolo, nazikungunula makungwa, kotero kuti nthambizo zinkaoneka za mipyololo yoyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Tsono Yakobo anatenga nthambi zaziwisi za mitengo ya mkundi, alimoni ndi puleni nazisenda kuchotsa makungwa ake mpaka mtengo woyera wamʼkati kuonekera.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:37
6 Mawu Ofanana  

Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.


Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa.


inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;


Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona nthyole ya katungurume.


Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa