Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Eksodo 4:17 - Buku Lopatulika Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Utenge ndodo ili m'manja mwakoyo, ukachite nayo zozizwitsa ndodo imeneyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.” |
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.
Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.
Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;