Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 4:17 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

17 Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Utenge ndodo ili m'manja mwakoyo, ukachite nayo zozizwitsa ndodo imeneyo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:17
8 Mawu Ofanana  

Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”


Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma.


Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”


Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”


Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.


“Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.”


Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa