Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Eksodo 30:4 - Buku Lopatulika Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo uzilumikize ku guwa m'munsi mwa mkombero pa mbali ziŵiri, kuti mphiko zipisidwe m'mphetezo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo. |
Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.
Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa.
Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.
Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.