Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.
Eksodo 30:10 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.” |
Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.
Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.
Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira.
nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.
Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.
Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.
Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.
Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;
koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;
Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu,