Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 4:18 - Buku Lopatulika

18 Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Pambuyo pake magaziwo aŵapake pa nyanga za guwa limene lili m'chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala aŵathire patsinde pa guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:18
11 Mawu Ofanana  

Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza paguwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi paguwa la nsembe; anaphanso anaankhosa aja, nawaza mwazi paguwa la nsembe.


Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.


Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.


Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;


Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.


Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.


Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.


Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa