Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 16:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono atatuluka Aroniyo apite ku guwa limene lili pamaso pa Chauta ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ng'ombe yamphongo ndiponso a mbuzi, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwalo molizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 16:18
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.


Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo, naupake pa mphuthu za Kachisi, ndi pangodya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za chipata cha bwalo lam'kati.


nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao.


Ndipo musakhale munthu m'chihema chokomanako pakulowa iye kuchita chotetezera m'malo opatulika, kufikira atuluka, atachita chotetezera yekha, ndi mbumba yake, ndi msonkhano wonse wa Israele.


Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.


Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu.


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa