Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:7 - Buku Lopatulika

7 koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma m'chipinda chachiŵiri chija ndi mkulu wa ansembe onse yekha amene amaloŵamo, nayenso ndi kamodzi kokha pa chaka, ndipo saloŵamo popanda kutenga magazi. Magaziwo ngokapereka kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini, ndiponso chifukwa cha machimo ochita anthu mosazindikira bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:7
23 Mawu Ofanana  

Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.


Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.


Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.


Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.


Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.


Anthu anga awavuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akuchimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo.


Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.


Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola lake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera chifukwa cha kusachimwa dala kwake, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.


Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;


Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.


odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;


Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.


chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;


amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.


Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa