Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Malinga ndi malongosoledwe ameneŵa, ansembe amaloŵa m'chipinda choyamba chija masiku onse pokagwira ntchito zao za chipembedzo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:6
9 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.


Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.


Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.


ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;


Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa