Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:8 - Buku Lopatulika

8 Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera akuphunzitsa kuti njira yoloŵera m'Malo Opatulika Kopambana ndi yosatsekukabe pamene chipinda choyamba chija chilipobe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:8
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ake, nati, Ali kuti Iye amene anawatulutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao,


Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.


Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.


Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,


Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.


kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.


Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,


Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,


Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;


pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa