Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 3:11 - Buku Lopatulika

Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele m'Ejipito?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo Mose adafunsa kuti, “Kodi ndine yani ine, kuti ndingapite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraele ku Ejipito?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Mose anafunsa Mulungu, “Ine ndine yani kuti ndipite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto?”

Onani mutuwo



Eksodo 3:11
13 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano?


Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.


Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.


koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?


si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka mu Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.


Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani mu Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?