Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 18:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani mu Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani m'Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono Davide adafunsa Saulo kuti, “Kodi ine ndine yani, ndipo abale anga ndi banja la bambo wanga ndife yani m'dziko la Israele, kuti ine nkukhala mkamwini wa mfumu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 18:18
9 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano?


Ahimaazi ku Nafutali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomoni;


Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?


Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.


Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa