Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 3:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma Mose anafunsa Mulungu, “Ine ndine yani kuti ndipite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele mu Ejipito?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele m'Ejipito?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo Mose adafunsa kuti, “Kodi ndine yani ine, kuti ndingapite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraele ku Ejipito?”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:11
13 Mawu Ofanana  

Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati: “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?”


“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi.


Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”


“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu.


Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?”


Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”


Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?


Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu.


Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.”


Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa