Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.
Eksodo 24:7 - Buku Lopatulika Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.” |
Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.
Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Yehova Mulungu wa Israele atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kutuluka m'nyumba ya ukapolo, kuti,
Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu?
Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.
Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.