Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 4:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 4:16
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,


Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;


Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli.


Perekani moni kwa abalewo a mu Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.


Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.


Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa