Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 42:6 - Buku Lopatulika

6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kaya nzabwino, kaya zoipa, tidzamvera ndithu mau a Chauta Mulungu wathu, amene takutumani kuti mukampemphe kanthu m'dzina lathu. Tidzamvera Chauta Mulungu wathu, kuti zinthu zitiyendere bwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 42:6
16 Mawu Ofanana  

Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.


Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.


Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.


Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao.


Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.


Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.


koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.


Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo.


Pamenepo tidzatani? Kodi chilamulo chili uchimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire;


Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.


Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.


Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!


Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.


Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa