Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.
Eksodo 22:31 - Buku Lopatulika Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.” |
Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.
Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.
Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.
Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.
Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.
koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.
Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.