Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 9:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Aisraele ena ndi ana ao aamuna adayamba kukwatira ana aakazi a anthuwo. Motero mtundu wathu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a m'maikowo. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo amene akupambana pa kusakhulupirika kumeneku.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”

Onani mutuwo Koperani




Ezara 9:2
24 Mawu Ofanana  

kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.


Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;


Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.


Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.


kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatirana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?


Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?


Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.


ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.


Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.


ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.


Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi mu Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.


Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.


Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.


Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?


Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.


Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Koma, mukadzabwerera m'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa