Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
Eksodo 22:14 - Buku Lopatulika Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati munthu abwereka chiweto cha mnzake ndipo chiweto chija nʼkuvulala kapena kufa chikanali ndi iyebe, wobwerekayo ayenera kulipira. |
Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.
Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.
Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova.