Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:15 - Buku Lopatulika

15 Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma ngati mwini wakeyo ali ndi chiwetocho, wobwerekayo sadzalipira. Ngati anapereka ndalama pobwereka chiwetocho, ndalama anaperekazo zilowa mʼmalo mwa chiweto chakufacho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:15
5 Mawu Ofanana  

Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.


Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.


Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake.


Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.


pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa