Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:4 - Buku Lopatulika

4 Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Panali enanso amene ankati, “Ife tachita kukongola ndalama kuti tikhome msonkho wa minda yathu kwa mfumu, ndiponso kuti tikhomere mitengo yathu yamphesa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:4
9 Mawu Ofanana  

ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.


Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mzinda uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m'kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.


Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi.


Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.


Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.


Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa