Nehemiya 5:5 - Buku Lopatulika5 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu aakazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsonotu ife ndi anzathu aja ndife amodzi, ndipo ana athu ngofanafana ndi ana ao. Komabe ifeyo tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo, mwakuti ana athu ena aakazi agwidwa kale. Ifeyo tilibe mphamvu zoti nkuchitapo kanthu, poti anthu aja atenga kale minda yathu ndi mitengo yathu yamphesa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.” Onani mutuwo |