Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;
Eksodo 22:11 - Buku Lopatulika lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndiye kuti anthu awiriwo ayenera kulumbira pamaso pa Mulungu kuti asatenge chinthu cha mnzake. Zikatero mwini katundu uja avomereze zimenezi ndipo asabwezeredwe kanthu. |
Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;
Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;
kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;
Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.