Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:10 - Buku Lopatulika

10 Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Ngati munthu wina anasungitsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa, kapena chiweto chilichonse ndipo chiweto chija nʼkufa kapena kupweteka kapena kutengedwa popanda wina kuona,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:10
6 Mawu Ofanana  

Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga;


lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.


Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.


Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.


Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona?


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa