Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:9 - Buku Lopatulika

9 Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:9
17 Mawu Ofanana  

Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.


Ngati munthu akachimwira mnzake, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba ino;


Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'mizinda mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.


Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;


Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.


kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.


Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.


Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.


Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa