Eksodo 22:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri. Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 “Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza. Onani mutuwo |
Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.