ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.
Eksodo 2:20 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa ana ake akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Nanga iyeyo ali kuti? Chifukwa chiyani mwamsiya komweko munthu ameneyo? Pitani mukamuitane, adzadye nao kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.” |
ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.
Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.
Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo.
Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.
Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.
Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.