Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.” Ndipo iwo anamuyankha nati, “Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.


Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa tsindwi langa.


Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.


Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.


ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.


Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;


Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.


Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikuchedwetseni kuti tikukonzereni mwanawambuzi.


Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova.


Ndipo kunali, tsiku lachinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kuchoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wake, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.


Musachoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kutulutsa chopereka changa ndi kuchiika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.


Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa