Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Abrahamu adaloŵa msangamsanga m'hema, nauza Sara kuti “Utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:6
15 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.


Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.


Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.


Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake.


Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.


Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.


Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa